Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Munthu akatuluka zotupa, kapena nkhanambo,+ kapena chikanga pakhungu lake, ndipo chasintha n’kukhala nthenda ya khate,+ azibwera naye kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake amenenso ndi ansembe.+

  • Levitiko 13:49
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 49 ndipo nthendayo ikuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pachovala kapena pachikopa, m’litali kapena m’lifupi mwa nsalu, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo iyenera kusonyezedwa kwa wansembe.

  • Levitiko 14:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Ili likhale lamulo lokhudza wakhate+ pa tsiku limene adzam’bweretsa kwa wansembe kudzagamulidwa kuti ndi woyera.+

  • Deuteronomo 24:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Samalani ndi mliri wa khate+ ndi kuonetsetsa kuti mukuchita zonse zimene ansembe achilevi adzakulangizani.+ Muzichita mosamala zonse zimene ndawalamula.+

  • Mateyu 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi,+ koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke mphatso+ imene Mose analamula, kuti ikhale umboni kwa iwo.”

  • Luka 5:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako analamula munthuyo kuti asauze aliyense.+ Ndiyeno anamuuza kuti: “Koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke nsembe+ ya kuyeretsedwa kwako, monga mmene Mose analamulira, kuti ikhale umboni kwa iwo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena