Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 22:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Anthu onse ondiona amandinyodola.+

      Iwo amandinyogodola ndi pakamwa pawo, ndipo amapukusa mitu yawo mondinyoza.+ Iwo amati:

  • Salimo 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Agalu andizungulira.+

      Khamu la anthu ochita zoipa landizinga.+

      Iwo akuluma manja ndi mapazi anga ngati mkango.+

  • Salimo 34:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Amateteza mafupa onse a wolungamayo.

      Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+

  • Salimo 69:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye,+

      Ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.+

  • Salimo 118:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Mwala umene omanga nyumba anaukana+

      Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+

  • Yesaya 50:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+

  • Yesaya 53:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+

  • Yesaya 53:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+ Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo,+ ndipo chifukwa cha zilonda zake+ ifeyo tachiritsidwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena