2 Ndiyeno mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova pamodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu onse okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ aneneri, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu.+ Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku+ la pangano+ limene linapezeka m’nyumba ya Yehova.+