19Tsopano angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pachipata cha Sodomu.+ Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+
35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+