Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+
Chilichonse mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.+
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
Ndipo usaiwale zochita zake zonse.+
3 Tamanda amene akukukhululukira zolakwa zako zonse,+
Iye amene akukuchiritsa matenda ako onse.+
4 Tamanda amene akuwombola moyo wako kudzenje,+
Amene akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu,+
5 Amene akukukhutiritsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.+
Mulungu akukuchititsa kukhalabe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+
6 Yehova akuchitira chilungamo+
Ndi kuperekera zigamulo anthu amene akuchitiridwa zachinyengo.+
7 Anauza Mose njira zake,+
Ndipo anadziwitsa ana a Isiraeli zochita zake.+
8 Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo,+
Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+
9 Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu,+
Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+
10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+
Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+
11 Pakuti monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,+
Kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.+
12 Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+
Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+
13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+
Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+
14 Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira,+
Amakumbukira kuti ndife fumbi.+
15 Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu wobiriwira.+
Iye amaphuka ngati mmene duwa lakutchire limaphukira.+
16 Mphepo ikawomba limafa,+
Ndipo pamalo amene linali sipadziwikanso,+
17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale,+
Kwa anthu amene amamuopa.+
Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+
18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu osunga pangano lake,+
Ndi kwa anthu okumbukira malamulo ake ndi kuwatsatira.+
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+
Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+
20 Tamandani Yehova, inu angelo+ ake amphamvu, ochita zimene wanena,+
Mwa kumvera malamulo ake.+
21 Tamandani Yehova inu makamu ake onse,+
Inu atumiki ake onse ochita chifuniro chake.+
22 Tamandani Yehova inu ntchito zake zonse,+
M’malo onse amene iye akulamulira.+
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+