Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.
2 Ndimvetsereni mwatcheru ndi kundiyankha.+
Mtima wanga suli m’malo chifukwa cha mavuto anga,+
Sindingachitire mwina koma kusonyeza nkhawa zanga,
3 Chifukwa cha zimene adani akunena, ndiponso chifukwa chakuti oipa andipanikiza.+
Pakuti akundikhuthulira mavuto,+
Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+
Ndikanapita kukakhala m’chipululu.+ [Seʹlah.]
8 Ndikanathawira kumalo opulumukirako,
Kuthawa mphepo yamphamvu, ndithu kuthawa mphepo yamkuntho.”+
9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani zonena zawo,+
Pakuti ndaona ziwawa ndi mikangano mumzinda.+
10 Usana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.+
Ndipo mumzindawo muli zopweteka ndi masautso.+
12 Pakuti amene ananditonza si mdani.+
Akanakhala mdani ndikanapirira.
Amene anadzikweza pamaso panga si munthu wodana nane kwambiri.+
Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.+
13 Koma ndiwe, munthu wofanana ndi ine,+
Munthu amene ndimam’dziwa bwino ndiponso mnzanga weniweni,+
14 Chifukwa tinali mabwenzi apamtima.+
Tinali kuyenda limodzi ndi khwimbi la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.+
17 Usiku, m’mawa ndi masana ndimakhala ndi nkhawa ndipo ndimakhala ndikulira,+
Choncho Mulungu amamva mawu anga.+
18 Iye adzandiwombola ndi kundikhazika pa mtendere, kundichotsa pankhondo,+
Pakuti khamu la anthu landiukira.+
19 Mulungu amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale,+
Adzandimvera ndipo adzawayankha,+ [Seʹlah.]
Anthu osafuna kusintha makhalidwe awo oipa,+
Ndiponso amene saopa Mulungu.+