Maliro
א [ʼAʹleph]
ב [Behth]
2 Ana okondedwa a Ziyoni+ amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengeka bwino,
Tsopano ayamba kuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi, ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.+
ג [Giʹmel]
3 Ngakhale mimbulu imapereka bere kwa ana ake kuti ayamwe.
Koma mwana wamkazi wa anthu anga wakhala wankhanza+ ngati nthiwatiwa m’chipululu.+
ד [Daʹleth]
ה [Heʼ]
5 Anthu amene anali kudya zinthu zabwino adzidzimuka ndipo agwidwa ndi mantha m’misewu.+
Anthu amene akula akuvala zovala zamtengo wapatali*+ agona pamilu ya phulusa.+
ו [Waw]
6 Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira chifukwa cha zolakwa zake, n’chachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+
Mzinda umenewu unawonongedwa mwadzidzidzi m’kanthawi kochepa, ndipo palibe dzanja limene linauthandiza.+
ז [Zaʹyin]
7 Anaziri+ ake anali oyera kuposa chipale chofewa.+ Analinso oyera kuposa mkaka.
Ndipotu anali ofiira+ kuposa miyala yamtengo wapatali ya korali. Analinso osalala ngati mwala wa safiro.+
ח [Chehth]
8 Tsopano ayamba kuoneka akuda kuposa makala. Anthu sakuwazindikiranso mumsewu.+
Khungu lawo lafota moti lamamatira kumafupa awo.+ Langoti gwaa ngati mtengo.
ט [Tehth]
9 Amene anaphedwa ndi lupanga+ aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala,+
Pakuti amene anafa ndi njala anafooka chifukwa chosowa chakudya, ndipo anakhala ngati apyozedwa ndi lupanga.
י [Yohdh]
10 Ngakhale amayi, amene amakhala achifundo, afika pophika ana awo ndi manja awo.+
Anawo akhala ngati chakudya chotonthoza anthu pa nthawi ya kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
כ [Kaph]
11 Yehova wasonyeza ukali wake wonse.+ Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+
Iye wayatsa moto m’Ziyoni, umene wanyeketsa maziko ake.+
ל [Laʹmedh]
12 Mafumu a padziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,+
Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pazipata za Yerusalemu.+
מ [Mem]
13 Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+
Amene anakhetsa magazi a anthu olungama a mumzindawo.+
נ [Nun]
14 Ansembe ndi aneneriwo akungoyendayenda mumsewu ngati anthu akhungu.+ Aipitsidwa ndi magazi,+
Moti palibe amene akukhudza zovala zawo.+
ס [Saʹmekh]
15 Anthu akuwafuulira kuti: “Chokani! Ndinu odetsedwa!+ Chokani! Chokani! Musatikhudze!”+
Ansembe ndi aneneriwo alibe pokhala+ ndipo akungoyendayenda.+ Anthu a mitundu ina akunena kuti: “Amenewa sapitiriza kukhala kuno.+
פ [Peʼ]
16 Yehova wawabalalitsa+ ndipo sadzawayang’ananso.+
Anthu sadzaganiziranso ansembe.+ Sadzachitiranso chifundo amuna okalamba.”+
ע [ʽAʹyin]
17 Pamene tili ndi moyo, maso athu akulefuka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+
Pofunafuna thandizo, tadalira mtundu wa anthu amene sangabweretse chipulumutso.+
צ [Tsa·dhehʹ]
18 Akutisakasaka kulikonse kumene tikupita,+ moti palibe amene akuyenda m’mabwalo a mizinda yathu.
Mapeto athu ayandikira. Masiku athu akwanira, pakuti mapeto athu afika.+
ק [Qohph]
ר [Rehsh]
20 Wodzozedwa wa Yehova,+ amene ndi mpweya wotuluka mphuno mwathu,+ wagwidwa m’dzenje lawo lalikulu.+
Ponena za ameneyu, ife tinati: “Tidzakhala mumthunzi wake+ pakati pa mitundu ya anthu.”+
ש [Sin]
21 Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+
Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+
ת [Taw]