Ekisodo
31 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Inetu ndikuitana ndi kutchula dzina Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndipo ndidzam’patsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse.+ 4 Ndidzam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,+ 5 waluso lolemba pamiyala mochita kugoba+ ndi wodziwa kupanga zinthu zina zilizonse zamatabwa.+ 6 Ndipo inetu ndaika Oholiabu mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani+ kuti athandize Bezaleli. Komanso ndaika nzeru mumtima wa munthu aliyense waluso, kuti apange zonse zimene ndakulamulazi:+ 7 chihema chokumanako,+ likasa+ la umboni, chivundikiro chimene chili pamwamba pake,+ ndi zipangizo zonse za m’chihema. 8 Kutinso apange tebulo ndi zipangizo zake,+ choikapo nyale chagolide woyenga bwino ndi zipangizo zake zonse,+ guwa lansembe zofukiza,+ 9 guwa lansembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse,+ beseni ndi choikapo chake,+ 10 zovala zosokedwa bwino ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe,+ 11 mafuta odzozera, ndi zofukiza zonunkhira za pamalo opatulika.+ Iwo adzapanga zonse malinga ndi zimene ndakulamula.”
12 Kenako Yehova anauzanso Mose kuti: 13 “Koma iwe uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti muzisunga masiku anga a sabata,+ pakuti ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu m’mibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.+ 14 Muzisunga sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Amene walinyoza ayenera kuphedwa ndithu.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la sabata adzaphedwa ndithu. 16 Ana a Isiraeli azisunga sabata, ndipo azichita zimenezi m’mibadwo yawo yonse. Limeneli ndi pangano mpaka kalekale.+ 17 Chimenechi n’chizindikiro pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa m’masiku 6, Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo pa tsiku la 7 anapuma pa ntchito yake.’”+
18 Ndiyeno atamaliza kulankhula naye paphiri la Sinai, anapatsa Mose miyala iwiri yosema ya Umboni,+ miyala yolembedwapo mawu ndi chala cha Mulungu.+