2 Mbiri
17 Ndiyeno Yehosafati+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli. 2 Iye anaika magulu ankhondo m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Anamanganso midzi ya asilikali m’dziko la Yuda ndi m’mizinda ya Efuraimu imene Asa bambo ake analanda.+ 3 Yehova anapitiriza kukhala ndi Yehosafati+ chifukwa anayenda m’njira zimene Davide kholo lake+ anayenda kalekale, ndipo sanafunefune Abaala.+ 4 Iye anafunafuna Mulungu wa bambo ake+ ndipo anayenda+ motsatira chilamulo chake, sanatsatire zochita za Aisiraeli.+ 5 Yehova anachititsa kuti ufumuwo ukhazikike m’manja mwake+ ndipo Ayuda onse anapitiriza kupereka+ mphatso kwa Yehosafati. Chotero iye anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka.+ 6 Komanso analimba mtima potsatira njira+ za Yehova ndipo anachotsa m’dziko la Yuda malo okwezeka+ ndi mizati yopatulika.+
7 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, anaitana akalonga ake kuti aziphunzitsa m’mizinda ya Yuda. Akalongawo anali Beni-hayili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya, 8 pamodzi ndi Alevi. Aleviwo anali Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yehonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobi-adoniya, pamodzi ndi ansembe Elisama ndi Yehoramu.+ 9 Iwo anayamba kuphunzitsa+ mu Yuda pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.+ Ankayendayenda m’mizinda yonse ya Yuda n’kumaphunzitsa anthu.
10 Mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira maufumu onse a m’mayiko ozungulira Yuda, ndipo sanachite nkhondo ndi Yehosafati.+ 11 Afilisiti anali kubweretsa+ mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho.+ Aluya+ nawonso anali kum’bweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi mbuzi zamphongo 7,700.+
12 Zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino Yehosafati ndipo mphamvu zake zinapitiriza kukula kwambiri.+ Iye anayamba kumanga m’dziko la Yuda malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ ndiponso mizinda yosungirako zinthu.+ 13 Panali zinthu zambiri m’mizinda ya Yuda zimene zinakhala zake. Ku Yerusalemu anali ndi asilikali,+ amuna amphamvu+ ndi olimba mtima. 14 Awa ndiwo anali maudindo awo potsata nyumba ya makolo awo: Adinala anali mmodzi wa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 a fuko la Yuda. Iye anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 300,000.+ 15 Adinalayo ankayang’anira Yehohanani mkulu wa asilikali, yemwe anali ndi asilikali 280,000. 16 Iye ankayang’aniranso Amasiya mwana wa Zikiri, yemwe anadzipereka kutumikira+ Yehova. Amasiyayo anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 200,000. 17 Kuchokera m’fuko la Benjamini+ panali Eliyada, mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima yemwe anali ndi asilikali 200,000 onyamula mauta ndi zishango.+ 18 Iye ankayang’anira Yehozabadi yemwe anali ndi asilikali 180,000 okonzekera kumenya nkhondo. 19 Amenewa ndiwo anali kutumikira mfumu, kuwonjezera pa anthu amene mfumuyo inawaika m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ m’dziko lonse la Yuda.