Masalimo
Masikili.* Salimo la Etani wa m’banja la Zera.+
89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+
Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+
2 Pakuti ndanena kuti: “Kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhazikika mpaka kalekale.+
Ndipo mwakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba.”+
3 Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+
Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga,+
4 ‘Ndidzakhazikitsa mbewu yako mpaka kalekale,+
Ndipo ndidzalimbitsa mpando wako wachifumu+ ku mibadwomibadwo.’” [Seʹlah.]
5 Inu Yehova, kumwamba kudzatamanda ntchito zanu zodabwitsa.+
Mpingo wa oyera anu udzatamanda kukhulupirika kwanu.
6 Pakuti ndani kumwamba angayerekezeredwe ndi Yehova?+
Ndani angafanane ndi Yehova pakati pa ana a Mulungu?+
7 Mulungu ayenera kuopedwa pakati pa gulu lake la oyera.+
Iye ndi wamkulu ndi wochititsa mantha kuposa onse omuzungulira.+
8 Inu Yehova Mulungu wa makamu,+
Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+
Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+
10 Mwaphwanya Rahabi*+ ndi kumuchititsa kukhala ngati munthu amene waphedwa.+
Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+
11 Kumwamba ndi kwanu,+ dziko lapansi nalonso ndi lanu.+
Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu.+
12 Munapanga kumpoto ndi kum’mwera.+
Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amafuula mokondwera ndi kutamanda dzina lanu.+
14 Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando wanu wachifumu.+
Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zili pamaso panu.+
15 Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala.+
Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova.+
18 Pakuti chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,+
Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+
19 Pa nthawi imeneyo munalankhula ndi okhulupirika anu mwa masomphenya,+
Ndipo munati:
“Ndapereka thandizo kwa wamphamvu.+
Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+
20 Ndapeza Davide mtumiki wanga,+
Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+
21 Dzanja langa lolimba lidzakhala pa iye.+
Mkono wanga udzamulimbitsa.+
22 Palibe mdani amene adzamupondereza,+
Ndipo palibe mwana aliyense wa anthu oipa amene adzamusautsa.+
23 Ndinaphwanya adani ake zidutswazidutswa ndi kuwachotsa pamaso pake,+
Ndipo odana naye kwambiri ndinapitirizabe kuwamenya.+
24 Kukhulupirika kwanga ndi kukoma mtima kwanga kosatha kuli pa iye,+
Ndipo nyanga yake imakwezedwa m’dzina langa.+
27 Inenso ndidzamuika kukhala mwana woyamba kubadwa,+
Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse a padziko lapansi.+
28 Ndidzamusonyeza kukoma mtima kwanga kosatha mpaka kalekale,+
Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+
29 Ndidzakhazikitsa mbewu yake kwamuyaya,+
Ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo kwa masiku ochuluka ngati masiku a kumwamba.+
30 Ana ake akadzasiya chilamulo changa,+
Ndi kuleka kutsatira zigamulo zanga,+
31 Akadzanyoza mfundo zanga,
Ndi kusasunga malamulo anga,
32 Ine ndidzawaimba mlandu ndi kuwalanga ndi ndodo,+
Ndipo ndidzawalanga ndi zikoti chifukwa cha zolakwa zawo.+
33 Koma kukoma mtima kwanga kosatha sindidzakuchotsa pa iye,+
Ndipo sindidzasiya kukhulupirika kwanga.+
36 Mbewu yake idzakhala mpaka kalekale,+
Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa pamaso panga.+
37 Udzakhazikika ngati mwezi mpaka kalekale,
Udzakhala ngati mboni yokhulupirika ya m’mlengalengayo.” [Seʹlah.]
39 Mwakana moipidwa pangano la mtumiki wanu.
Mwanyoza chisoti chake chachifumu mwa kuchiponyera pansi.+
41 Onse oyenda njira imeneyo afunkha zinthu zake.+
Iye wakhala chinthu chotonzedwa kwa anthu oyandikana naye.+
43 Kuwonjezera apo, mukuonanso lupanga lake ngati mdani,+
Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo.+
46 Inu Yehova, kodi mudzadzibisa kufikira liti? Ku nthawi zonse?+
Kodi mkwiyo wanu udzakhalabe ukuyaka ngati moto?+
48 Kodi pali mwamuna wamphamvu aliyense amene sadzaona imfa?+
Kodi angathe kupulumutsa moyo wake m’dzanja la Manda?+ [Seʹlah.]
49 Kodi zochita zanu zakale zija zosonyeza kukoma mtima kosatha zili kuti, inu Yehova?
Zija zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+