Yoswa
11 Ndiyeno Yabini mfumu ya ku Hazori+ atangomva nkhaniyi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni, ndi mfumu ya ku Simironi, ndiponso mfumu ya ku Akasafu.+ 2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amene anali m’dera lamapiri kumpoto, ndiponso m’chipululu kum’mwera kwa nyanja ya Kinereti,*+ mafumu a ku Sefela,+ ndiponso kwa mafumu okhala m’mapiri a Dori+ kumadzulo. 3 Anaitanitsanso Akanani+ okhala kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso Aamori,+ Ahiti,+ Aperezi+ ndi Ayebusi+ okhala kudera lamapiri. Komanso anaitanitsa Ahivi+ omwe anali kukhala m’munsi mwa phiri la Herimoni+ ku Mizipa.+ 4 Choncho mafumuwo pamodzi ndi magulu awo onse ankhondo ananyamuka. Anali anthu ambiri, kuchuluka kwawo ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo anali ndi mahatchi*+ ambiri zedi komanso magaleta* ankhondo. 5 Mafumu onsewa anakumana pamodzi monga anapanganirana. Ndiyeno onse pamodzi anakamanga msasa pafupi ndi madzi a ku Meromu kuti akamenyane ndi Aisiraeli.+
6 Pamenepo Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ pakuti mawa pa nthawi ngati yomwe ino, ndidzawapereka onsewo kuti aphedwe ndi Aisiraeli. Mahatchi awo udzawapundula,*+ ndipo magaleta awo udzawatentha ndi moto.”+ 7 Yoswa ndi asilikali ake onse anapita kufupi ndi madzi a Meromu ndi kuthira nkhondo adaniwo modzidzimutsa. 8 Ndipo Yehova anapereka adaniwo m’manja mwa Aisiraeli.+ Chotero anayamba kuwapha ndi kuwathamangitsa mpaka kukafika kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe+ kum’mawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+ 9 Pambuyo pake Yoswa anachita zimene Yehova anamuuza. Mahatchi awo anawapundula,+ ndipo magaleta awo anawatentha ndi moto.+
10 Kuwonjezera apo, Yoswa anabwerera ndi kukalanda+ mzinda wa Hazori+ n’kupha mfumu yake ndi lupanga.+ Anachita zimenezi chifukwa mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa. 11 Aisiraeliwo anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo.+ Panalibe chamoyo chilichonse chimene chinatsala,+ ndipo Yoswa anatentha mzinda wa Hazori ndi moto. 12 Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, ndi kugwira mafumu onse a mizindayi n’kuwapha ndi lupanga.+ Anawawononga onsewo+ monga mmene analamulira Mose mtumiki wa Yehova.+ 13 Mizinda yonse imene inamangidwa pamabwinja a mizinda yakale, Aisiraeli sanaitenthe ndi moto, kupatulapo mzinda wa Hazori umene Yoswa anautentha ndi moto. 14 Ana a Isiraeli anafunkha katundu yense wa m’mizindayi ndi ziweto zomwe.+ Koma anthu anawapha ndi lupanga kufikira atawamaliza onse.+ Sanasiye munthu aliyense wamoyo.+ 15 Monga Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamula Yoswa,+ ndipo Yoswayo anachitadi zimenezo. Palibe mawu alionse amene Yoswa anasiya pa mawu onse amene Yehova analamula Mose.+
16 Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni,+ ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake.+ 17 Analandanso dera lochokera kuphiri la Halaki+ lomwe lili moyang’anizana ndi Seiri+ mpaka kukafika ku Baala-gadi,+ kuchigwa cha Lebanoni m’munsi mwa phiri la Herimoni.+ Yoswa anagwira mafumu awo onse ndi kuwapha.+ 18 Iye anachita nkhondo ndi mafumu onsewa kwa masiku ambiri. 19 Panalibe mzinda winanso umene unapangana za mtendere ndi ana a Isiraeli kupatulapo Ahivi+ okhala mumzinda wa Gibeoni.+ Ana a Isiraeli analanda mizinda ina yonse mwankhondo.+ 20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+
21 Kuwonjezera apo, pa nthawiyo Yoswa anapita n’kukafafaniziratu Aanaki.+ Aanakiwo anali kukhala kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi,+ kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli.+ Yoswa anafafaniziratu Aanakiwo pamodzi ndi mizinda yawo.+ 22 M’dziko la ana a Isiraeli, palibe Aanaki amene anatsalamo,+ kupatulapo okhala ku Gaza,+ ku Gati+ ndi ku Asidodi.+ 23 Chotero Yoswa analanda dziko lonse monga mmene Yehova analonjezera Mose.+ Ndiyeno Yoswa anapereka dzikolo kwa Aisiraeli monga cholowa chawo, malinga ndi magawo awo potsata mafuko awo.+ Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+