Deuteronomo
8 “Muonetsetse kuti mukusunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndi kuti muchulukanedi, n’kupita kukatenga dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.+ 2 Muzikumbukira njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani m’chipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa,+ kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mukanasunga malamulo ake kapena ayi. 3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokukhalitsani ndi njala+ ndi kukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sanawadziwe. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse ochokera m’kamwa mwa Yehova.+ 4 Zovala zanu sizinathe ndipo mapazi anu sanatupe m’zaka 40 zimenezi.+ 5 Inu mukudziwa bwino mumtima mwanu kuti Yehova Mulungu wanu anali kukuwongolerani, ngati mmene bambo amawongolerera mwana wake.+
6 “Muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu mwa kuyenda m’njira zake+ ndi kumuopa.+ 7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani m’dziko labwino,+ dziko la zigwa* za madzi,+ akasupe ndi madzi ochuluka otuluka m’zigwa ndi m’madera a mapiri, 8 dziko la tirigu, balere, mphesa, nkhuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+ 9 dziko limene mudzadya mkate wosaperewera, limenenso simudzasowa kalikonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso m’mapiri ake mudzakumbamo mkuwa.
10 “Mukadzadya ndi kukhuta+ mudzatamandenso+ Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+ 11 Samalani kuti musaiwale+ Yehova Mulungu wanu ndi kusasunga malamulo, zigamulo ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero.+ 12 Samalani, kuopera kuti mungadye ndi kukhuta, kumanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,+ 13 ng’ombe zanu ndi nkhosa zanu n’kuchuluka, siliva ndi golide wanu n’kuwonjezeka ndiponso zinthu zanu zonse n’kukuchulukirani, 14 mtima wanu n’kuyamba kudzikweza+ ndi kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 15 Mungaiwale amene anakuyendetsani m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni,+ zinkhanira ndiponso dziko louma lopanda madzi. Amenenso anakutulutsirani madzi pamwala wolimba ngati nsangalabwi.+ 16 Mungaiwale amene anakudyetsani mana+ m’chipululu, chakudya chimene makolo anu sanachidziwe, pofuna kukuphunzitsani kudzichepetsa+ ndi kuti akuyeseni kuti potsirizira pake akuchitireni zabwino.+ 17 Samalani kuti munganene mumtima mwanu kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza ndi mphamvu zanga ndi nyonga za dzanja langa.’+ 18 Muzikumbukira Yehova Mulungu wanu, chifukwa ndiye amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbirira makolo anu, monga mmene wachitira lero.+
19 “Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu, n’kutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchitirani umboni lero kuti anthu inu mudzatha.+ 20 Mudzatheratu ngati mitundu imene Yehova akuiwononga pamaso panu, chifukwa simudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.+