1 Yohane
5 Onse amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, ndi ana a Mulungu,+ ndipo onse amene amakonda Atate amakondanso mwana wake.+ 2 Tikamakonda+ ana a Mulungu,+ ndiye kuti tikukonda Mulungu ndiponso tikusunga malamulo ake.+ 3 Chifukwa kukonda+ Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo+ ndi osalemetsa.+ 4 Onse amene ali ana+ a Mulungu amagonjetsa dziko.+ Ndipo tagonjetsa+ dziko ndi chikhulupiriro chathu.+
5 Kodi ndani amene amagonjetsa+ dziko?+ Kodi si amene amakhulupirira+ kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?+ 6 Ameneyu ndi Yesu Khristu, amene anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi. Sanabwere kudzera mwa madzi+ okha, koma anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi.+ Ndipo mzimu+ ndi umene ukuchitira umboni, chifukwa mzimu ndiwo choonadi. 7 Pakuti pali mboni zitatu, 8 mzimu,+ madzi,+ ndi magazi,+ ndipo zitatuzi n’zogwirizana.+
9 Ngati timakhulupirira umboni umene anthu amapereka,+ n’zoonekeratu kuti umboni umene Mulungu amapereka ndi woposa umboni wa anthu. Timakhulupirira umboni wa Mulungu chifukwa chakuti amachitira umboni+ za Mwana wake. 10 Munthu wokhulupirira Mwana wa Mulungu ndiye kuti walandira umboni+ umene wapatsidwa. Munthu wosakhulupirira Mulungu ndiye kuti akumuona ngati wonama,+ chifukwa sanakhulupirire kuti zimene Mulungu wanena+ zokhudza Mwana wake, ndi zoona.+ 11 Umboni umene waperekedwa ndi wakuti, Mulungu anatipatsa moyo wosatha,+ ndipo tinaulandira kudzera mwa Mwana wake.+ 12 Munthu amene wavomereza Mwana ndiye kuti ali ndi moyo umenewu ndipo amene sanavomereze Mwana wa Mulungu alibe moyo umenewu.+
13 Ndikukulemberani izi kuti mudziwe kuti inu amene mumakhulupirira m’dzina la Mwana wa Mulungu+ muli ndi moyo wosatha.+ 14 Ifetu timamudalira+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.+ 15 Komanso, popeza timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse,+ timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.+
16 Ngati wina waona m’bale wake akuchita tchimo losabweretsa imfa,+ amupempherere, ndipo Mulungu adzamupatsa moyo.+ Panotu ndikunena za ochita machimo osabweretsa imfa.+ Koma palinso tchimo lobweretsa imfa. Ndipo sindikunena kuti mupempherere munthu amene wachita tchimo loterolo.+ 17 Kusalungama kulikonse ndi tchimo.+ Komabe pali tchimo limene silibweretsa imfa.
18 Tikudziwa kuti munthu aliyense amene ali mwana wa Mulungu+ sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, koma mwana*+ wa Mulungu amamuyang’anira, ndipo woipayo samugwira.+ 19 Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu,+ koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.+ 20 Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anabwera,+ ndipo anatipatsa nzeru+ kuti timudziwe woonayo.+ Ndipo ife ndife ogwirizana+ ndi woonayo, kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona+ ndiponso wopereka moyo wosatha.+ 21 Inu ana okondedwa, pewani mafano.+