1 Yohane
4 Okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa,+ koma muziyesa mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokeradi kwa Mulungu,+ chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.+
2 Kuti tidziwe ngati mawu ali ouziridwa ndiponso ochokera kwa Mulungu,+ timadziwira izi: Mawuwo amavomereza zoti Yesu Khristu anabwera monga munthu.+ 3 Koma mawu alionse ouziridwa amene amatsutsa zoti Yesu anabwera monga munthu, amenewo si ochokera kwa Mulungu,+ ndipo ndi ouziridwa ndi wokana Khristu amene munamva kuti akubwera,+ ndipo tsopano ali kale m’dziko.+
4 Ana okondedwa, inu ndinu ochokera kwa Mulungu, ndipo mwagonjetsa anthu amenewo,+ chifukwa amene muli ogwirizana+ naye ndi wamkulu+ kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.+ 5 Iwo ndi ochokera m’dziko,+ n’chifukwa chake amalankhula zochokera m’dziko ndipo dziko limawamvera.+ 6 Ife ndife ochokera kwa Mulungu.+ Amene amadziwa Mulungu amatimvera,+ ndipo amene sachokera kwa Mulungu satimvera.+ Mmenemu ndi mmene timadziwira mawu ouziridwa oona kapena abodza.+
7 Okondedwa, tiyeni tipitirize kukondana,+ chifukwa chikondi+ chimachokera kwa Mulungu,+ ndipo aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu ndipo akudziwa Mulungu.+ 8 Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.+ 9 Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake+ pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha+ kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.+ 10 Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe+ yophimba+ machimo athu.+
11 Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tiyenera kukondana.+ 12 Palibe amene anaonapo Mulungu.+ Tikapitiriza kukondana, Mulungu apitiriza kukhala mwa ife ndipo chikondi chake kwa ife chikhala chokwanira.+ 13 Tikudziwa kuti ndife ogwirizana+ naye, ndiponso iye ndi wogwirizana ndi ife+ chifukwa watipatsa mzimu wake.+ 14 Komanso ife taona+ ndipo tikuchitira umboni+ kuti Atate anatumiza Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko.+ 15 Aliyense amene amavomereza kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu,+ amakhala wogwirizana ndi Mulungu ndipo Mulungu amakhala wogwirizana naye.+ 16 Ife tikudziwa ndipo tikukhulupirira za chikondi+ chimene Mulungu ali nacho kwa ife.
Mulungu ndiye chikondi,+ ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi,+ amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana+ naye. 17 Chikondi chimenechi chakhala chokwanira kwa ife kuti tidzathe kulankhula momasuka+ m’tsiku lachiweruzo,+ chifukwa mmene Yesu Khristu alili, ndi mmenenso ife tilili m’dzikoli.+ 18 M’chikondi mulibe mantha,+ koma chikondi chimene chili chokwanira chimathetsa mantha,+ chifukwa mantha amachititsa munthu kukhala womangika. Amene ali ndi mantha, chikondi chake si chokwanira.+ 19 Koma ife timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.+
20 Ngati wina amanena kuti: “Ndimakonda Mulungu,” koma amadana ndi m’bale wake, ndiye kuti ndi wabodza.+ Pakuti amene sakonda m’bale wake+ amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.+ 21 Ndipo iye anatipatsa lamulo ili lakuti,+ munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.+