Ezekieli
9 Kenako iye analankhula mokuwa ine ndikumva, kuti: “Uzani anthu amene asankhidwa kuti awononge mzindawu kuti abwere pafupi. Aliyense anyamule chida chake chowonongera.”
2 Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kuchipata chakumtunda+ choyang’ana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chophwanyira. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu.+ M’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati n’kuima pambali pa guwa lansembe lamkuwa.+
3 Tsopano ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi+ pamene unali, ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Kenako Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu wovala zovala zansalu uja,+ yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera. 4 Pamenepo Yehova anauza munthu uja kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu, ndipo ulembe chizindikiro pamphumi za anthu amene akuusa moyo* ndi kubuula+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.”+
5 Ndiyeno iye anauza amuna ena aja ine ndikumva, kuti: “M’tsatireni ameneyu. Muyendeyende mumzindamo n’kumapha anthu. Diso lanu lisamve chisoni ndipo inuyo musachite chifundo.+ 6 Mupheretu nkhalamba, anyamata, anamwali, tiana, ndi amayi.+ Koma musayandikire munthu aliyense amene ali ndi chizindikiro,+ ndipo muyambire pamalo anga opatulika.”+ Chotero iwo anayambira kupha akuluakulu amene anali panyumbapo.+ 7 Iye anawauzanso kuti: “Ipitsani nyumbayi ndipo mudzaze mabwalo ake ndi mitembo ya anthu ophedwa.+ Pitani!” Iwo anapitadi n’kukapha anthu mumzindamo.
8 Pamene amunawo anali kupha anthu, ine ndinatsala ndekha wamoyo, ndipo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinafuula kuti: “Kalanga ine,+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi muwononga otsala onse a Isiraeli pamene mukukhuthulira ukali wanu pa Yerusalemu?”+
9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+ 10 Chotero inenso diso langa silimva chisoni+ ndipo sindichita chifundo.+ Ndiwabwezera mogwirizana ndi njira zawo.”+
11 Tsopano munthu wovala zovala zansalu uja, yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera, anabwera n’kudzanena kuti: “Ndachita monga momwe munanditumira.”+