Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
4 Inu Mulungu, mwazunguliridwa ndi kuwala, ndipo ndinu wochititsa nthumanzi kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.+
5 Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo,+
Iwo awodzera ndi kugona tulo,+
Ndipo palibe ngakhale mmodzi mwa anthu onse olimba mtimawo amene ali ndi mphamvu zotsutsa.+
6 Hatchi komanso wokwera galeta agona tulo tofa nato chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo.+
8 Munachititsa ziweruzo zanu kumveka kuchokera kumwambako.+
Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala duu+
9 Pamene Mulungu ananyamuka ndi kupereka chiweruzo,+
Kuti apulumutse anthu onse ofatsa padziko lapansi.+ [Seʹlah.]