Miyambo
9 Nzeru yeniyeni+ yamanga nyumba yake.+ Yasema zipilala zake 7. 2 Yapha nyama yake ndipo yasakaniza vinyo wake. Kuwonjezera apo, yayala patebulo pake.+ 3 Yatuma antchito ake aakazi kuti apite pamwamba pa zitunda za m’mudzi akaiitanire anthu, kuti: 4 “Aliyense wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense wopanda nzeru mumtima mwake,+ nzeru* ikumuuza kuti: 5 “Bwerani mudzadye chakudya changa ndiponso mudzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.+ 6 Alekeni anthu osadziwa zinthu kuti mupitirize kukhala ndi moyo,+ ndipo yendani mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.”+
7 Amene amalangiza wonyoza amadzichotsera yekha ulemu,+ ndipo amene amadzudzula woipa amadzibweretsera chilema.+ 8 Usadzudzule wonyoza kuti angadane nawe.+ Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+ 9 Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+ Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.
10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+ 11 Pakuti ine ndidzachititsa kuti masiku ako akhale ambiri+ ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.+ 12 Ngati wakhala wanzeru, nzeruzo zidzapindulitsa iweyo.+ Ngati uli wonyoza, iweyo ndiye udzavutike.+
13 Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+ Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.+ 14 Wakhala pampando pakhomo la nyumba yake, pachitunda cha m’mudzimo,+ 15 kuti aziitana anthu odutsa amene akuyenda panjira zawo atalunjika kutsogolo. Iye akuwauza kuti:+ 16 “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense amene ali wopanda nzeru mumtima mwake,+ mkaziyo wamuuza kuti: 17 “Madzi akuba amatsekemera,*+ ndipo mkate wakudya mwakabisira umakoma.”+ 18 Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa, ndiponso kuti amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.+