Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
19 Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+
Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+
4 Zingwe zawo zoyezera zafika padziko lonse lapansi,+
Mawu awo amveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+
Kumwambako Mulungu wamangira dzuwa hema.+
5 Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka m’chipinda chake,+
Limakondwa ngati mmene mwamuna wamphamvu amachitira akamathamanga m’njira.+
6 Limatuluka kuchokera kumalekezero ena a kumwamba,
Ndi kuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+
Palibe chinthu chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.+
7 Chilamulo+ cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa moyo.+
Zikumbutso+ za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+
9 Kuopa+ Yehova n’koyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.
Zigamulo+ za Yehova n’zolondola,+ ndipo pa mbali iliyonse zasonyezadi kuti ndi zolungama.+
10 N’zolakalakika kuposa golide, kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+
N’zotsekemera* kuposa uchi,+ inde kuposa uchi umene ukukha m’zisa.+
12 Ndani angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+
Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.+