Masalimo
Nyimbo ndi Salimo la Davide.
101 Ndidzaimba za kukoma mtima kwanu kosatha ndi chiweruzo chanu.+
Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.+
2 Ndidzachita zinthu mwanzeru m’njira yowongoka.+
Kodi inu mudzandithandiza liti?+
Ndidzayendayenda m’nyumba yanga ndi mtima wanga wosagawanika.+
3 Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.+
Ndimadana ndi zochita za opatuka pa choonadi.+
Sindilola kuti zochita zawozo zindikhudze.+
5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+
Ndimamukhalitsa chete.+
Sindingathe kupirira zochita za+
Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+
6 Maso anga ali pa okhulupirika a padziko lapansi,+
Kuti akhale ndi ine.+
Woyenda m’njira yowongoka,+
Ndi amene adzanditumikira.+