Masalimo
3 Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+
Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati:
“Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+
6 Lilime langa limamatire m’kamwa mwanga+
Ngati sindingakukumbukire,+
Ngati sindingakweze iwe Yerusalemu
Pamwamba pa chilichonse chimene chimandikondweretsa.+
7 Inu Yehova, kumbukirani+ zimene ana a Edomu+ ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa,+
Iwo anati: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni mpaka pamaziko ake!”+