1 Atesalonika
5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo+ abale, simukufunika kukulemberani kanthu. 2 Pakuti inu eni mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.+ 3 Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+ 4 Koma inu abale simuli mu mdima ayi,+ kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.+ 5 Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala+ ndiponso ana a usana.+ Si ife a usiku kapena a mdima ayi.+
6 Chotero tisapitirize kugona+ ngati mmene enawo akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+ 7 Pakuti ogona+ amagona usiku,+ ndipo amene amaledzera amakonda kuledzera usiku. 8 Koma ife amene tili a usana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa+ chachikhulupiriro+ ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso+ monga chisoti,+ 9 chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti tidzaone mkwiyo.+ Anatisankha kuti tipeze chipulumutso+ kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 10 Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona, tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+ 11 Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ monga mmene mukuchitira.+
12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani+ mwa Ambuye ndi kukulangizani. 13 Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.+ Khalani mwamtendere pakati panu.+ 14 Komanso tikukudandaulirani abale kuti, langizani ochita zosalongosoka,+ lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni,+ thandizani ofooka, khalani oleza+ mtima kwa onse. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse yesetsani kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+
16 Muzikhala okondwera nthawi zonse.+ 17 Muzipemphera mosalekeza.+ 18 Muziyamika+ pa chilichonse, pakuti chimenechi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. 19 Musazimitse moto wa mzimu.+ 20 Musanyoze mawu aulosi.+ 21 Tsimikizirani zinthu zonse.+ Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.+ 22 Pewani zoipa zamtundu uliwonse.+
23 Mulungu wamtendere+ mwiniyo akupatuleni+ kuti muchite utumiki wake. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chilema ndi zopanda cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 24 Amene akukuitanani ndi wokhulupirika, ndipo adzachitadi zimenezi.
25 Abale, pitirizani kutipempherera.+
26 Perekani moni kwa abale onse ndi kupsompsonana kwaubale.+
27 Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+
28 Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.