3 Abulamu atachoka ku Negebu, ankamanga misasa malo osiyanasiyana nʼkumasamuka mpaka anakafika ku Beteli, kumene kunali tenti yake poyamba, pakati pa Beteli ndi Ai.+
2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni, kumʼmawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza mzindawu.” Amunawo anapita nʼkukafufuza zokhudza mzinda wa Ai.