-
Genesis 12:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Patapita nthawi, anasamuka pamalopo nʼkupita kudera lamapiri, kumʼmawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga tenti yake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kumʼmawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe+ nʼkuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+ 9 Pambuyo pake Abulamu anasamutsa tenti yake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+
-