Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzapangitsa kuti dzina lako litchuke. Komanso anthu ena adzadalitsidwa chifukwa cha iwe.+

  • Genesis 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu mʼmasomphenya kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+

  • Genesis 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+

  • Ekisodo 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Aisiraeli* anaberekana ndipo anachuluka kwambiri mʼdzikomo. Iwo anapitiriza kukhala amphamvu komanso anachulukana mofulumira kwambiri, moti anadzaza mʼdzikomo.+

  • Aheberi 11:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pa chifukwa chimenechi, kuchokera kwa mwamuna mmodzi, amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ambirimbiri+ ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena