Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 13:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Abulamu atasiyana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo.

  • Genesis 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndidzachulukitsa mbadwa zako* ngati mchenga wapadziko lapansi. Choncho ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbadwa zako* zidzatha kuwerengedwa.+

  • Genesis 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu mʼmasomphenya kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+

  • Genesis 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+

  • Genesis 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Dzina lako silikhalanso Abulamu* koma likhala Abulahamu,* chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri.

  • Genesis 22:17, 18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbadwa* zako ngati nyenyezi zakumwamba komanso ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.+ Ndipo mbadwa yako idzalanda mzinda* wa adani ake.+ 18 Kudzera mwa mbadwa* yako,+ mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+

  • Deuteronomo 26:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kenako muzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Bambo anga anali munthu wongoyendayenda wa Chiaramu*+ ndipo anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa amʼbanja lawo+ nʼkukakhala kumeneko monga mlendo. Koma ali kumeneko anakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena