-
Yoswa 24:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Pamene ndinkatulutsa makolo anu ku Iguputo,+ atatsala pangʼono kufika kunyanja, Aiguputo anawathamangira ndi magaleta ankhondo ndiponso amuna okwera pamahatchi, mpaka ku Nyanja Yofiira.+ 7 Iwo anayamba kufuulira Yehova.+ Choncho ndinaika mdima pakati pa iwo ndi Aiguputuwo, ndipo ndinawamiza ndi madzi amʼnyanja.+ Munaona ndi maso anu zimene ndinachita ku Iguputo.+ Kenako inu munakhala mʼchipululu zaka zambiri.*+
-