Genesis 15:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+ Ekisodo 38:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* Anthu onse amene anawerengedwa analipo 603,550.+ Numeri 1:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Anthu onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+ Numeri 14:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ Numeri 26:51 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 51 Amuna onse amene anawerengedwa pakati pa Aisiraeli ndi amenewa ndipo onse pamodzi analipo 601,730.+ Numeri 26:64 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 64 Koma pakati pa anthu amenewa, panalibe munthu aliyense amene anali mʼgulu la anthu omwe anawerengedwa mʼchipululu cha Sinai, nthawi imene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga Aisiraeli.+
5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+
26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* Anthu onse amene anawerengedwa analipo 603,550.+
29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+
51 Amuna onse amene anawerengedwa pakati pa Aisiraeli ndi amenewa ndipo onse pamodzi analipo 601,730.+
64 Koma pakati pa anthu amenewa, panalibe munthu aliyense amene anali mʼgulu la anthu omwe anawerengedwa mʼchipululu cha Sinai, nthawi imene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga Aisiraeli.+