-
Numeri 21:33-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Pambuyo pake, anatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndiyeno Ogi+ mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nawo ku Edirei.+ 34 Yehova anauza Mose kuti: “Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndipereka iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse komanso dziko lake mʼmanja mwako+ ndipo umuchitire zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni.”+ 35 Choncho Aisiraeliwo anapha iyeyo, ana ake ndi anthu ake onse, moti palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka,+ ndipo analanda dziko lake.+
-
-
Deuteronomo 3:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho Yehova Mulungu wathu anaperekanso Ogi mfumu ya Basana ndi anthu ake onse mʼmanja mwathu, ndipo tinawapha moti panalibe munthu ngakhale mmodzi mwa anthu ake, yemwe anapulumuka.
-