Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

      Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu?

      Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+

  • Deuteronomo 4:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndi Mulungu woona.+ Palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.+

  • Salimo 73:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Winanso ndi ndani kumwambako amene angandithandize?

      Ndipo chifukwa chakuti inu muli ndi ine, palibenso chimene ndimalakalaka padziko lapansi.+

  • Salimo 86:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+

      Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+

  • Salimo 89:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Ndi ndani kumwamba amene angafanane ndi Yehova?+

      Ndi ndani pakati pa ana a Mulungu+ amene ndi wofanana ndi Yehova?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena