Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+

  • Ekisodo 34:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+

  • Deuteronomo 12:5, 6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+

  • Yoswa 18:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kenako gulu lonse la Aisiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamanga chihema chokumanako,+ popeza pa nthawiyo nʼkuti atagonjetsa dzikolo.+

  • Oweruza 21:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Kenako anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka chilichonse. Mzinda wa Silo uli kumpoto kwa Beteli, chakumʼmawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kumʼmwera kwa Lebona.”

  • Luka 2:41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Chaka ndi chaka makolo ake ankakonda kupita ku Yerusalemu, kuchikondwerero cha Pasika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena