Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+

      Ndipo palibe Mulungu wina koma ine ndekha.+

      Ndimapha komanso ndimapereka moyo.+

      Ndimavulaza,+ ndipo ndidzachiritsa,+

      Palibe aliyense amene angapulumutse munthu mʼdzanja langa.+

  • Yobu 14:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Zikanakhala bwino mukanandibisa mʼManda,*+

      Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utadutsa,

      Zikanakhala bwino mukanandiikira nthawi nʼkudzandikumbukira.+

  • Salimo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Inu Yehova, mwanditulutsa mʼManda,*+

      Mwandisunga ndi moyo, mwanditeteza kuti ndisatsikire mʼdzenje.*+

  • Salimo 49:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma Mulungu adzandiwombola ku mphamvu ya* Manda,*+

      Chifukwa adzandigwira dzanja. (Selah)

  • Salimo 68:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+

      Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.+

  • Hoseya 13:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ine ndidzawombola anthu anga ku mphamvu za Manda.*

      Ndidzawapulumutsa ku imfa.+

      Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+

      Iwe Manda, kodi mphamvu yako yowononga ili kuti?+

      Koma Efuraimu sindimumvera chisoni.

  • Yohane 11:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Marita anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa+ mʼtsiku lomaliza.”

  • 1 Akorinto 15:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 “Iwe Imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe Imfa, amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena