-
1 Mbiri 17:11-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ukadzamwalira nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mmodzi wa ana ako,+ akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+ 12 Iye ndi amene adzandimangire nyumba+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 13 Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Sindidzamuchotsera chikondi changa chokhulupirika+ ngati mmene ndinachitira kwa munthu yemwe analipo iwe usanakhalepo.+ 14 Ndidzamuchititsa kuti akhale woyangʼanira nyumba yanga ndi ufumu wanga mpaka kalekale,+ ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo mpaka kalekale.”’”+
-
-
Salimo 132:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Yehova walumbira kwa Davide.
Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti:
-
-
Yesaya 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ulamuliro* wake udzafika kutali
Ndipo mtendere sudzatha,+
Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake
Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba
Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.
-