Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+

  • 2 Samueli 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ukadzamwalira+ nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mwana wako weniweni, akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+

  • Salimo 132:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova walumbira kwa Davide.

      Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti:

      “Ndidzaika pampando wako wachifumu

      Mmodzi wa ana ako.*+

  • Yesaya 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Ulamuliro* wake udzafika kutali

      Ndipo mtendere sudzatha,+

      Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake

      Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba

      Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+

      Kuyambira panopa mpaka kalekale.

      Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.

  • Yesaya 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nthambi+ idzaphuka pachitsa cha Jese,+

      Ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzabereka zipatso.

  • Yesaya 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa tsiku limenelo muzu wa Jese+ udzaimirira ngati chizindikiro kwa anthu.+

      Anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awapatse malangizo,*+

      Ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Mateyu 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Buku la mzere wa makolo a Yesu Khristu,* mwana wa Davide,+ mwana wa Abulahamu:+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena