-
1 Mafumu 19:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Atafika kumeneko, analowa mʼphanga+ nʼkugona mmenemo usiku wonse. Kenako anamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Ukudzatani kuno Eliya?” 10 Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+ koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+
-