-
Ekisodo 30:12-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Ukamachita kalembera wa ana a Isiraeli,+ aliyense azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi imene ukuwawerengayo. Azichita zimenezi kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo. 13 Anthu onse amene awerengedwa azipereka zinthu izi: hafu ya sekeli* yofanana ndi sekeli yakumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli imodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+ 14 Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo azipereka chopereka kwa Yehova.+ 15 Mukamapereka kwa Yehova chopereka chophimba machimo kuti muwombole moyo wanu, anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.* 16 Uzilandira ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa Aisiraeli nʼkuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapachihema chokumanako. Ndalama zimenezi zidzathandiza kuti Yehova azikumbukira Aisiraeli komanso zidzaphimba machimo anu kuti muwombole moyo wanu.”
-