Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Mukabwereketsa ndalama kwa munthu aliyense wosauka* pakati pa anthu anga, kwa munthu amene ali pafupi ndi inu, musakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira kwa iye. Musamuuze kuti apereke chiwongoladzanja.+

  • Deuteronomo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja pa ndalama,+ chakudya kapena pa chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja.

  • Salimo 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

      Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

      Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.*+

  • Ezekieli 22:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mwa iwe muli anthu amene akulandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe ukabwereketsa ndalama umafuna kuti akupatse chiwongoladzanja+ kapena kuti upeze phindu* ndipo ukubera anzako ndalama mwachinyengo.+ Ndithu, ine wandiiwaliratu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena