Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi mosamala kwambiri,+ chifukwa mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti ndinu anzeru+ komanso ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa ndipo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi komanso ozindikira.’+

  • Salimo 111:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Chiyambi cha nzeru ndi kuopa Yehova.+

      ש [Sin]

      Onse otsatira malamulo ake amasonyeza kuti ndi ozindikira.+

      ת [Taw]

      Iye ayenera kutamandidwa mpaka kalekale.

  • Miyambo 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru,+

      Ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa,+ udzakhala womvetsa zinthu.

  • Mlaliki 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndi zimene munthu akuyenera kuchita.+

  • Aroma 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa,+ ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu wake,+ zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena