Salimo 20:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova akuyankheni pa tsiku la mavuto. Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+ Salimo 79:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+ Miyambo 18:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.*+
9 Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+