17 Yehova, Wokuwombolani, Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti:
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu,
Amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+
Amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda.+
18 Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+
Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje+
Ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a mʼnyanja.+