-
Yesaya 33:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndi amene amayenda mʼchilungamo nthawi zonse,+
Amene amalankhula zoona,+
Amene amakana kupeza phindu pochita zinthu mosaona mtima komanso mwachinyengo,
Amene manja ake amakana chiphuphu, mʼmalo mochilandira,+
Amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi,
Ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zinthu zoipa.
16 Iye adzakhala pamalo okwera.
Malo ake othawirako otetezeka* adzakhala mʼmatanthwe movuta kufikamo.
Iye adzapatsidwa chakudya
Ndipo madzi ake sadzatha.”+
-