Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 40:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Inu Yehova Mulungu wanga,

      Mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa+

      Ndipo mumatiganizira.+

      Palibe angafanane ndi inu.

      Nditati ndilankhule kapena kunena za zodabwitsazo,

      Zingakhale zochuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

  • Salimo 145:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo.

      Adzanena za ntchito zanu zamphamvu.+

  • Mlaliki 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chilichonse iye anachipanga chokongola* ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Komabe anthu sadzadziwa ntchito imene Mulungu woona wagwira kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto.

  • Chivumbulutso 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iwo ankaimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu ndi nyimbo ya Mwanawankhosa+ yakuti:

      “Ntchito zanu nʼzazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova* Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama komanso zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena