44 Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+