Salimo 92:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Ndipo adzalengeza kuti Yehova ndi wolungama. Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama. Salimo 119:68 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 68 Inu ndinu wabwino+ ndipo ntchito zanu ndi zabwino. Ndiphunzitseni malamulo anu.+ Salimo 145:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova ndi wabwino kwa aliyense,+Ndipo ntchito zake zonse zimasonyeza kuti ndi wachifundo. Machitidwe 14:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+
17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+