-
Deuteronomo 28:49, 50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
49 Yehova adzatumiza mtundu wakutali+ kuchokera kumalekezero adziko lapansi kuti udzakuukireni. Mtunduwo udzakuukirani mofulumira kwambiri ngati mmene chiwombankhanga chimagwirira nyama.+ Mtundu umenewo chilankhulo chake simudzachimva,+ 50 mtundu wooneka moopsa umene sudzamvera chisoni munthu wachikulire kapena kuchitira chifundo mnyamata.+
-
-
Yeremiya 4:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Mahatchi ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+
Tsoka latigwera chifukwa tawonongedwa.
-
-
Habakuku 1:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Umene umathamanga mʼmadera ambiri apadziko lapansi,
Kukalanda nyumba zimene si zawo.+
-
-
Habakuku 1:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Mahatchi ake ankhondo amathamanga kwambiri.
Mahatchi awo amachokera kutali.
Ndipo amauluka ngati chiwombankhanga chimene chikuthamanga kuti chikapeze chakudya.+
-