9 Inu mumasamalira dziko lapansi,
Mumalichititsa kuti libale zipatso zambiri komanso kuti likhale lachonde.+
Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wodzadza ndi madzi.
Mumachititsa kuti dziko lapansi lipereke chakudya kwa anthu,+
Umu ndi mmene dziko lapansi munalipangira.