Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Danieli 4:13-16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndikuona masomphenyawo ndili pabedi langa, ndinaona mlonda, mthenga woyera akutsika kuchokera kumwamba.+ 14 Mlondayo analankhula mofuula kuti: “Gwetsani mtengowo+ ndipo mudule nthambi zake. Yoyolani masamba ake ndipo mumwaze zipatso zake. Nyama zithawe pansi pake ndipo mbalame zichoke panthambi zake. 15 Koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo komanso wakopa.* Chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chikhalenso pakati pa nyama zakutchire ndi udzu wapadziko lapansi.+ 16 Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu nʼkukhala mtima wa nyama ndipo padutse+ nthawi zokwana 7.+

  • Luka 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu mpaka nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena