-
Danieli 4:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Inu munaona mtengo umene unakula kwambiri ndipo unakhala wamphamvu. Nsonga ya mtengowo inakafika mpaka kumwamba ndipo unkaoneka padziko lonse lapansi.+ 21 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira anthu ndi nyama zonse. Nyama zakutchire zinkakhala pansi pake ndipo mbalame zamumlengalenga zinkakhala munthambi zake.+ 22 Mtengowo ndi inuyo mfumu, chifukwa mwakula ndipo mwakhala wamphamvu. Ulemerero wanu wakula mpaka kukafika kumwamba+ ndipo ulamuliro wanu wafika kumalekezero a dziko lapansi.+
-