-
2 Petulo 3:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yachiwiri imene ndikukulemberani, ndipo mofanana ndi yoyamba ija, ndikukulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito bwino mphamvu zanu zoganiza pokukumbutsani zimene mukudziwa kale.+ 2 Ndikuchita zimenezi kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kalero komanso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu anapereka kudzera mwa atumwi.*
-