-
1 Mafumu 17:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 “Nyamuka, upite ku Zarefati mʼdziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wamasiye kuti azikakupatsa chakudya.”+ 10 Choncho Eliya ananyamuka nʼkupita ku Zarefati. Atafika pageti la mzindawo anaona mayi wamasiye akutola nkhuni. Ndiyeno anamuitana nʼkumuuza kuti: “Mundipatseko madzi pangʼono mʼkapu kuti ndimwe.”+
-
-
1 Mafumu 17:20-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Kenako anafuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga,+ kodi mukuchitiranso zoipa mayi wamasiye amene ndikukhala nayeyu pomuphera mwana wake?” 21 Ndiyeno anakumbatira mwanayo katatu ali pabedipo nʼkufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere.” 22 Yehova anamva pemphero la Eliya+ ndipo moyo wa mwanayo unabwerera moti anakhalanso wamoyo.+ 23 Eliya anatenga mwanayo nʼkutsika naye kuchokera mʼchipinda chapadenga chija ndipo anapita naye kwa mayi ake. Ndiyeno anati: “Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”+
-
-
2 Mafumu 4:13-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno Elisa anauza Gehazi kuti: “Muuze kuti, ‘Mwavutika ndi kutisamalira,+ kodi tingakuchitireni chiyani?+ Kodi pali chinachake choti tikakunenereni kwa mfumu,+ kapena kwa mkulu wa asilikali?’” Koma mayiyo anayankha kuti: “Ayi, palibe. Ndikukhala mwamtendere ndi anthu a mtundu wanga.” 14 Elisa anati: “Ndiye timuchitire chiyani?” Gehazi anayankha kuti: “Mayiyutu alibe mwana wamwamuna+ ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.” 15 Nthawi yomweyo Elisa anati: “Muitane.” Choncho Gehazi anamuitana ndipo mayiyo anaima pakhomo. 16 Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Ayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.”
17 Komabe, mayiyo anakhala ndi pakati nthawi ngati yomweyo chaka chotsatira ndipo anabereka mwana wamwamuna mogwirizana ndi zimene Elisa anamuuza.
-