18 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe+19 ndipo akamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amuchitire chipongwe, kumukwapula ndi kumupachika pamtengo+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza Mtumiki wake+ Yesu,+ amene inu munamupereka+ ndiponso kumukana pamaso pa Pilato, ngakhale kuti Pilatoyo ankafuna kumumasula.